Gulu la Fashion and Glams lapereka katundu wokwana 1.2Million kwacha kuti bungwe lomenyera ufulu wa anthu a mtundu wachialubino la Association with People with Albinism (APAM) .
M`modzi mwa membala wa guluri Fawzia Osman wati ndalamazi azipeza kudzera muzochitikachitika zomwe guluri linachititsa ndicholinga chopeza ndalama zothandizira anthu amtundu wa chialubino m`dziko muno.
Mwazina, katunduyi ndi zipewa zomwe zimathandiza athuwa kupherela mphamvu ya dzuwa.
Ndipo m`mawu ake mkulu wa bungwe la APAM, OverstoneKondowe wathokoza guluri kamba kathandizoli lomwe ladza munthawi yake ndipo walonjeza kuti lifika kwa anthu amtunduwu m`madera onse m`dziko muno.