Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Episkopi Apempha Akhristu Atsatire Moyo Wa Francis Wa Ku Assisi Woyera

$
0
0

Akhristu a mpingo wa katolika m’dziko muno awapempha kuti akhale olimba pa chikhristu chawo komanso achifundo kwa ovutika monga ankachitira Francis wa ku Assisi woyera.

Poyankhula pa mwambo womwe parishi ya St. Francis of Assisi Chidzanja mudayosizi ya Mangochi imachita chaka chokondwelera nkhoswe yake episkopi wa dayosiziyi ambuye Montfort stima anati mu moyo wa francis wa ku assisi woyera akhristu akuyenera kutengapo phunziro lalikulu lomwe akuyenerakutsatapa chikhristu chawo.

“Moyo wa francis ukutiuza kuti iye sanatenge chuma cha kwawo ngati chinthu chake chake koma anagwiritsa ntchito mwayi umenewu wa chuma cha makolo ake pothandizira ovutika ndi osowa. Atatero makolo ake anamukwiyira kuti awabwezere chuma chawo koma iye sadafooke adalimbabe mtima. Choncho nafenso akhristu ndi kangachepe kamene tili nako tikuyenera kusonyeza chifundo kwa anzathu amene akusowa komanso tikhale olimba mtima pa chikhristu chathu ngakhale tikumane ndi zowawa,”anatero ambuye Stima.

Patsikuli ambuye Stima anaperekanso sacrament la ulimbitso kwa akhristu okwana 167 a mparishiyi. M’mawu awo ambuye stima apempha akhristu omwe alimbitsidwa kumenewa kuti asalekele pompa koma adzipereke ku mpingo polowa magulu osiyanasiyana a mumpingowu.

“Pamene alimbitsidwa chonchi sikuti apherezera ayi. Tikufuna aziphunzirabe pa sabata kamodzikomanso alowemmagulu osiyanasiyana a mumpingomwathu mu. Zimenezitikufuna kuti ana athuwa apitilire kuzama mu chikhristu makamu chiphunzitso cha mpingo wa eklezia katolika,”anatero ambuye Stima.

Polankhulapopa mwambowubambo mfumu a parishiyi bamboKizito Khauyaapempha akhristu omwe alandira sacrament la ulimbitso pa tsikuli kuti akhale olimba pa chikhristu chawo.

Iwo anati, “Imodzi mwa mphatso za mzimu woyera zomwe munthu amalandira pa ulimbitso ndi chamuna cha chikhristu. Ndiye tikuwapempha kuti akhale olimba pa chikhristu chawo.”

Parishi ya Chidzanja ndi imodzi mwa parishi zisanu zomwe zinakhazikitsidwa mu dayosiziyi m’mwezi wa July chaka chatha ndi episkopi wa dayosiziyi Ambuye Montfort Stima.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>