Amayi mpingo wakatolika kwa Chikapa mu Parish ya Nthawira mu arki dayosizi ya Blantyre awayamikira kamba kolimbikitsa ubale wabwino pakati pawo ndi amayi a ku parish ya Chisitu ku Mulanje mu arki dayosiziyo.
Bambo mfumu a parish ya Chisitu, Bambo Lawrence Simbota ndi omwe anena izi pothililapo ndemanga pa ulendo omwe amayiwa anakonza wokacheza ndi amayi anzawo ku parishi ya Chisiti.
Bambo Simbota ati zomwe amayiwa achita zalimbikitsa ubale wabwino pakati pa amayi m’maparishi awiriwa.
Polankhulanso wa pa mpando wa bungwe la amayi-wa kwa Chikapa mayi Agness Kalonga ati ulendowu anawukonzanso ndi cholinga choti akacheze ndi Bambo Lawrence Simbota mwa zaka zam’buyomuakhalanso akutumikira parish yawo ya Nthawira.