Makhansala mdziko muno awapempha kuti azigwira ntchito yobweretsa chitukuko m’ma ward mwawo kuti anthu amene anawasankha aziwakhulupilira.
Khansala wa ward ya Sadzi mu mzinda wa Zomba mayi Mercy Chaputula ndi yemwe wanena izi pamene amatsekulira chitukuko cha mpopi mderali.
Mayi Chaputula atsimikizira anthu mderali kuti agwira nawo ntchito limodzi kuti chitukuko chifalikire mdera lonse la Sadzi.
“Ichi ndi chitukuko changa choyamba chomwe ndinawalonjeza anthu anga ndalama zake ndi zochoka m’thumba mwanga. Ine ndigwira nawo limodzi ntchito anthu a m’dera langa komanso ndipemphe makhansala anzanga kuti tizichita zinthu zosiyanasiyana zomwe tinawalonjeza anthu athu,” anatero mayi Chaputula.
M’mawu ake wapampando wa bungwe la amayi mchigawo cha kum’mawa mchipani cholamula cha Democratic Progressive DPP, mayi Elube Kandewu athokoza khansala Chaputula kaamba kopereka chitukuko cha madzi kwa anthu a mdera la Sadzi ndipo apempha makhansala ena kuti atengerepo chitsanzo.