Anthu atatu afa ataomberedwa ndi bambo wina pa sukulu ina yomwe ili kumpoto kwa dera la San Bernardino mu mzinda wa Califonia mdziko la America.
Malipoti a wailesi ya BBC ati munthuyu anaombera ndikupha yemwe anali mkazi wake wakale, mphunzitsi wapasukulupo komanso mwana yemwe anali pamalopo ndi kuvulazanso ana ena. Munthuyu ati atamaliza kuchita izi anaziomberanso yekha.
Bambo-yu Cedric Anderson yemwe ndi wa zaka 53 zakubadwa ati panthawi-yo analowa pa sukulupo ngati mulendo ndipo anasunga mfuti yakeyo malo obisika.
Pakadali pano malipoti ati mwana yemwe anavulala kwambiri pa chiwembucho akupezako bwino ndipo ana ena omwe anasala pasukulupo awasamusira ku sukulu ina ya m’deralo.