Mtsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Francisco wapempha mtendere mdziko la Central African Republic potsatira zamtopola zomwe zikuchitika mdzikolo.
Papa amalankhula izi lamulungu ku likulu la mpingowu ku Vatican mdziko la Italy pambuyo pa mapemphero a m’mawa pa bwalo la St Peters.
Papa wati ndi okhudzidwa kwambiri kaamba ka zamtopola zomwe zikupitilira kuchitika mdzikolo pambuyo poliyendera mmwezi wa November mu chaka cha 2015. Iye wati zamtopola zomwe zikuchitika mdziko la CAR zachititsa kuti anthu ambiri amwalire, asowe pokhala komanso mtendere.
Pamenepa iye wati apitiriza kuwapemphelera anthuwa komanso onse omwe akuchita ntchito zachifundo zobweretsa mtendere pakati pa dzikolo.