M’tsogoleri wa dziko lino Professor Peter Muthalika wapempha anthu m’dziko muno kuti azipewa kusankhana mitundu kamba koti izi sizingathandize pa chitukuko cha dziko lino.
President Muthalika wanena izi mzinda wa Lilongwe utangotha mwambo wa mapemphero apadera othokoza Mulungu kamba zabwino zomwe akupitiliza kuchitira dziko lino kufikira pano pomwe lakwanitsa zaka 53 lili pa ufulu wodzilamulira.
Iye wati anthu m’dziko muno akuyenera kumatanganidwa ndi ntchito zotukula dziko lino kamba koti zimenezi ndi zomwe zingathandize pa chitukuko cha dziko lino.