Bungwe la za umoyo pa dziko lonse la World Health Organization (WHO) lati amayi akuyenera kumayamwitsa ana awo mkaka wa mmawere ndi cholinga choti anawo azikula ndi thanzi labwino.
Polankhula lachitatu pa 3RD August 2017 mu m’dzinda wa LILONGWE , mkulu woona za umoyo wa ana , komanso kadyedwe koyenera m’bungweli , DR SUZEN KAMBALE ati mu mkaka wa m’mawere mumakhala zonse zofunikira pa thanzi la mwana , zomwe zipangitsa kuti mwanayo azikula ndi thanzi labwino.
Iwo ati kuyamwitsa mwana mkaka wa m’mawere mwakathithi ndi moyenera kumathandiza kupewa matenda aku nyetchera pakati pa ana choncho amayi akuyenera kumatsatira bwino malangizo oyenerawa ndi kumayamwitsa ana mkaka wa m’mawere moyenera.