Episkopi wa Dayosizi ya Mangochi yampingo wakatolika Ambuye Montfort Sitima ati adzipeleka kothelatu pa ntchito zothandiza komanso kutumikira Radio Maria Malawi.
Episikopiyu amayankhula izi pomwe kwa nthawi yoyamba chimukhazikitsire pa udindowu anayendera likulu la wailesiyi lomwe lili mdayosizi ya Mangochi .
Paulendowu Ambuye Sitima acheza ndi anthu otumikira kuwailesiyi komanso kugawana mfundo zina zothandiza kupititsa pa tsogolo ntchito za wailesiyi.
“Ndiyesetsa kuthandiza ndikugwira nanu ntchito limodzi kuti tigwiritse ntchito wailesiyi momwe mwini ake Mulungu akufunira”anatero Ambuye Sitima.
M’mawu ake mkulu woyendetsa ntchito za ma programu a pa wailesiyi Bambo Joseph Kimu athokoza Ambuye Sitima chifukwa chokonza ulendo wodzacheza ndi otumikira ku wailesiyi.
Iwo apempha ambuyewa kuti akhale omasuka akapeza mthawi ndi kumafika ku nyumbayi kudzapanga nawo maprogramu ndi ntchito zina zothandiza pa chitukuko cha wailesiyi.