Moto wolusa wasaka nyumba 23 za anthu a m’mudzi mwa kafutula m’dera la mfumu yayikulu Nankhumba , m’boma la Mangochi.
M’modzi mwa anthu omwe akhudzidwa ndi ngozi-yi a Leonard Mbewe ati moto umene wasakaza nyumbazi unayatsidwa ndi mwana wina zaka 7 zakubadwa pomwe amachita masewera ake m’mudzimo .
Ambewe ati mwatsoka moto umene anakoleza mwanayu akuti unapezeka kuti wagwilira nyumba ina ya udzu yomwe amaonetseramo video kenaka ndi kuyambanso kugwilira nyumba zina zoyandikana ndi malowo.
Padakalipano katundu wa ndalama zoposera 16 Million Kwacha akuti ndi amene akumuganizira kuti wapsa ndi motowo ndipo wina mwa katundu-yi ndi monga chakudya zofunda ndi zina zambiri.
Malingana ndi ofalitsa nkhani za apolisi m’bomalo inspector Rodrick Maida pa ngoziyi palibe amene wavulala.