Apolisi mu mzinda wa New Delhi mdziko la India,aletsa ziwonetsero zomwe akhristu a mpingo wakatolika anakonza mumzindawo pokwiya ndi ziwembu zomwe anthu ena akumachitira matchalitchi a mpingowu mdzikolo.
Mkwiyo wa anthuwo wakula kwambiri, boma litakananso kupereka zitupa zokhalira mdzikolo kwa akuluakulu awiri ochokera ku likulu la mpingowu ku Vatican, omwe akufuna kufika mdzikolo kukatsogolera msonkhano okambirana dongosolo la chipembedzo, omwe ukuyembekezeka kuchitika mdzikolo sabata ya mawa.
Archepiskopi Arthur Roche yemwe ndi mlembi owona za chipembedzo, komanso Archepiskopi Portase Rugambwa yemwe ndi mkulu oyendetsa ntchito za mabungwe a utumiki wa apapa kulikululo alepheretsa ulendowo atamva zoti sapatsidwa zitupazo.
Pakadali pano, bungwe la maepiskopi mdzikolo lati likakamiza boma kuti lifotokoze bwino chifukwa chomwe lakanira kupereka zitupazo kwa akuluakuluwo.