Zigawenga za mgulu la Islamic State I.S, zalengeza kuti zanyonga akhristu makumi awiri ndi mmodzi a mdziko la Egypt,omwe zidawagwira mdziko la Libya kumayambiliro a mwezi wa January chaka chino.
Lipoti lomwe gululo latulutsa pa makina a intaneti lati zigawengazo zachita chiwembucho, pobwezera imfa ya amayi ena achisilamu omwe adaphedwa mwankhanza mdziko la Egypt.
Padakali pano,dziko la Egypt silidatsimikize kuti akhristuwo ndi a mdzikolo, koma lati lili ndi mantha aakulu oti anthuwo atha kukhala a mdzikolo.