Mwambo woyika mmanda asisteri awiri Sister Chrissy Govati ndi Sister Martha Clemence Manuel Makhasa a Chipani cha Servants of the Blessed Virgin Mary wachitika lolemba ku Mary View ku Nguludi mu Archdayosizi ya Blantyre.
Mwambowu unatsogoleredwa ndi nsembe ya misa yomwe anatsogolera ndi Arch-Episkopi wa dayosiziyi Ambuye Thomas Luke Msusa. Ambuye Msusa ati iwo ndi wokhudzidwa kwambiri kamba ka imfa ya masisteri awiriwa. Iwo ati imfa ya masisteriwa yachepetsa chiwerengero cha atumiki a mulungu mchipanichi.
Ku mwambowu kunafika ansembe, asisteri ndi akhristu ochokera mmadayosizi osiyanasiyana.
Malemu Sister Chrissy Govati anabadwa pa 14 September 1975, ku parishi ya Mtepuwa mmudzi mwa a Kang’oma kwa mfumu yayikulu Mabuka m’boma la Mulanje ndipo iwowa amwalira akutumikira ku Parish ya Balaka, pomwe Sister Martha Clemence Manuel Makhasa anali wochokera m’mudzi wa Mbaisa kwa mfumu yayikulu Mpama m’boma la Chiradzulu, ku parish ya Masanjala ndipo iwowa amwalira ali ku nyumba yopuma ya asisteri a chipanichi ku Mary View ku Nguludi.