Mtsogoleri wa mpingo wa Katolika pa dziko lonse Papa Francisco akuyembekezeka kukumana ndi mtsogoleri wa dziko la America Barrack Obama mwezi wa September chaka chino.
Paulendowu Papa Francisco akuyembekezeka kukumana ndi Pulezidenti Obama komanso Mayi Michell Obama pa 23 September kunyumba ya boma mdzikolo, pamene akuyembekezeka kukambirana nkhani zosiyanasiyana.
Malinga ndi ofesi yofalitsa nkhani ku likulu la mpingo wa Katolika ku Vatican, atsogoleri awiriwa akuyembekezeka kukambirana nkhani zokhudza ufulu wachipembedzo, kusamalira zachilengedwe,osauka ndi zina zambiri zomwe adayamba kale kukambirana Pulezidenti Obama atakacheza ku likulu la mpingowu chaka chatha.