Dziko la South Africa lamanga anthu 17 ndipo ena mwa iwo lawatsekulira milandu yakupha paziwawa zomwe mzika za dzikolo zikuchita pokwiya ndi anthu a mmayiko ena omwe akugwira ntchito zosiyanasiyana mdzikolo maka mumzinda wa Durban.
Ziwawazo zayamba masiku apitawa,imodzi mwa mafumu akuluakulu mdzikolo itanena mawu oti anthu a mmaiko ena omwe akukhala mdzikolo abwelere mmaiko awo.
Mfumuyo ikukana zoti idalankhula mawuwa, ndipo yati anthu amene akukokomeza zoti iyo idalankhula izi sadamvetse bwino.
Mfumuyo yawuza akuluakulu a mpingo mdzikolo kuti ponena kuti anthu a mmaiko ena omwe akukhala mdzikolo abwelere mmaiko awo,inkatanthauza anthu amene alibe zitupa zoyenera kukhalira mdzikolo.
Nduna ya zamdziko mdzikolo yalangiza mafumu kuti adzipewa kulankhula zinthu zomwe zingadzetse ziwawa.
Anthu 62 omwe ena mwa iwo ndi mzika za dziko lino adaphedwa paziwawa ngati zomwezi mchaka cha 2008,pomwe amkakamizidwa kuti abwelere mmaiko awo.
Pakadali pano anthu oposa 250 ataya katundu wawo paziwawazi