Ofesi yofalitsa nkhani mu dayosizi ya Zomba yapempha anthu akufuna kwabwino kuti athandize dayosiziyi ndi zipangizo zogwilira ntchito ku studio ya Zomba ya Radio Maria ndi cholinga choti dayosiziyi ipitilize kujambula mapulogalamu osiyanasiyana.
Mkulu wamuofesiyi mu dayosiziyo bambo Steven Likhutcha anayankhula izi loweruka,pa ulendo wandawala omwe anthu otumikira wailesiyi kustudio ya Zomba anali nawo pofuna kupeza zipangizo zosiyanasiyana zofunikira kuti ntchito yojambula mapulogalamu kustudio-yo idzitheka.
Bambo Likhutcha ati pali zinthu zambiri zomwe zikufunika ku studio-yo, ndipo apempha mabungwe ndinso anthu ena akufuna kwabwino kuti achitepo kanthu popereka zomwe angakwanitse.
“Tikupemba kwa anthu amene ali ndi malaptop kuti atithandize ngakhalenso amene ali ndi luso lokonza zinthu zosiyanasiyana,”anatero Bambo Likhutcha.
Ulendo wa ndawalawo unayambira pamaofesi a Cadecom mumzinda wa Zomba, pomwenso pali studio ya wayilesiyi mpaka ku St Anthony parishi ku Thondwe, omwe ndi mtunda wa pafupifupi makilomita khumi ndi asanu.