Mwambo woyika mmanda thupi la malemu Sister Anastazia Mzaza a chipani cha Charity of Ottawa wachitika lolemba ku parish ya Ludzi m’boma la Mchinji.
Sister Anastazia Mzaza,anabadwa pa 10 November mchaka cha 1924,ndipo amwalira ali ndi zaka 91.
Iwo anachita malumbiro awo oyamba pa 16 June 1954,ndipo amwalira atatumikira mumpingowu kwa zaka 61.
Iwo akhala akutumikira ku parishi ya Ludzi, Mkanda komanso ku Kachebere mu arkdayosizi ya Lilongwe.