↧
Bambo wina wa zaka 40 zakubadwa wamwalira atawombedwa ndi mphenzi m’boma la Ntchisi.
Wofalitsa nkhani za apolisi m’bomalo Sergent Gladson M’bumpha watsimikiza za nkhaniyi.
Iye wati chiphaliwalichi chinadza kamba ka mvula ya mphamvu yomwe inagwa m’delalo masana a lachiwiri m’bomalo.
Malingana ndi a M’bumpha chiphaliwalicho chitamuwomba mkuluyi ati anthu anamutengera ku chipatala komwe malipoti anasonyeza kuti anali atamwalira kale.
Malemuyu Richard Banda anali wochokera m’mudzi wa Buleya kwa mfumu yaikulu Nkhombedza m’boma la Salima.