Atsogoleri atsopano a bungwe loyimira akhristu eni mu mpingo wakatolika awapempha kuti adzipeleke pa ntchito yolimbikitsa akhristu pa za mpingo wodzidalira.
Mlangizi wa bungwe-li mu mpingo wa katolika m’dziko muno ambuye Peter Musikuwa anena izi ku Lilongwe pa msonkhano wa atsogoleri-wa.
Ambuye Musikuwa omwenso ndi a episkopi a dayosizi ya Chikwawa ati padakalipano mpingo ukusowa zambiri zothandizira kuti ntchito zake zipitilire kuyenda bwino kamba koti ansembe achizungu omwe anali kuthandiza mpingowu mdziko muno anabwelera kwawo. Kotero akhristu amu mpingowu akuyenera kuphunzitsidwa bwino kuti adziwe zaudindo wawo pa chitukuko cha mpingo.
A kulikulu la mpingo wakatolika m’dziko muno ku Episcopal Conference of Malawi (ECM) ndi amene anakonzera atsogoleri-wa msonkhano-wu.