Bungwe loyendetsa zisankho m'dziko muno, la Malawi Electoral Commission,lati silidaike tsiku lodzachitira chisankho chachibwereza m'ndondomeko yakagwiridwe ka ntchito zake zokonzekera chisankho cha chaka cha mawa, opikisana atadzafanana mavoti, kaamba koti bungweli, silidaganizire za chisankho cha mtunduwu pokonza ndondomekoyi.
M'modzi mwa makomishonala a bungweli Mai Nancy Tembo, yemwenso ndi wapampando wa komiti yoyendetsa ntchito zophunzitsa anthu kubungweli, ndi yemwe wanena izi pomwe Radio Maria Malawi imafuna kudziwa chomwe chachititsa kuti bungweli, lisaike tsiku lochitira chisankho cha mtunduwu patapezeka kuti opikisana afanana mavoti. Komishonala Tembo wati bungweli, silidaganizire konse zachisankho cha mtunduwu pokonza ndondomekoyi, yomwe yakhazikitsidwa pa 14 mwezi uno.Iye wati nzokaikitsa kwambiri kuti padzakhala kufunika kochititsa chisankho chachibwereza, ndipo anatsimikizira anthu kuti patapezeka kuti opikisana afanana mavoti pachisankhochi,bungweli lidzachita chotheka kuti voti idzachitikenso mmaudindo okhawo okhudzaidwa.