Lero mpingo wakatolika umachita chaka cha odwala komanso cha Amayi Maria a ku Lourdes.
Tsikuli linakhazikitsidwa m`chaka cha 1992 ndi Papa Yohane Paulo wachiwiri ndipo mapemphero atsikuli chaka chino achitikira kutchalitchi cha Amayi Maria ku Arotin.
Cholinga cha tsikuli ndi kukumbutsa Akhristu kuti azipemphera molimbika ndikupemphelera odwala, kusinkhasinkha ndikuchitapo kanthu pothandiza odwala komanso kuyamikira onse amene amagwira ntchito yotumikira odwala.
Muuthenga wake chaka chino mkulu wampingo wa katolika padziko lonse lapansi Papa Benedikito wa 16 wapempha akhristu kuti aone ndikuzindikira nkhope yakhristu mwa abale ndi alongo amene akuvutika ndikusautsidwa kaamba ka mavuto osiyanasiyana komanso kuti azindikire pamene khristuyo adazunzidwa ndi kuuka kwa akufa adadzetsa chipulumutso kumtundu wonse wa anthu monga momwe adalembera Papa Yohane Paulo wachiwiri m`kalata yake yoyamba ya chaka cha odwala pa 13 may 1992.
Potsatira mutu wa chaka chino "Pitani Tsono Nanunso Muzikachita Chimodzimodzi" Luka 10:37, Apapa apempha anthu kuti asinkhesinkhe za fanizo la Msamaliya wachifundo lomwe ambuye yesu akutithandizira kuti timvetse mozama za chikondi cha Mulungu pamunthu wina aliyense makamaka paiwo amene akuzunzika ndi ululu komanso matenda osiyanasiyana .
"Akhristu akuyenera kuphunzira chikondi chamulungu kudzera pokhala naye muubale pakupemphera kwambiri pamoyo wawo watsikunditsiku kuti adzikhudzidwa kwambiri monga adachitira Msamaliya wa chifundo", watero Papa Benedikito wa 16.
Apapawa afuniranso zabwino zonse anthu onse amene akukumana ndizokhoma panthawi imene akusamalira odwala.
"Ndikufuna kukulimbitsani mtima inu abale anga ndi mawu a nthumwi zakunsonkhano wa Vatikani kuti simulinokha, simunataike, simunalekereledwe komanso sindinu opanda pake , akuthunzitseni mtima mwaitanidwa ndi khristu ndipo ndinu chithunzi chamoyo wake", watero Papa Benedikito wa 16.