Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

MTSOGOLERI WA MPINGO WAKATOLIKA ATULA PANSI UDINDO WAKE

$
0
0

 

Mtsogoleri wa mpingo wakatolika padziko lonse lapansi Papa Benedikito wa 16 walengeza kuti atula pansi udindo wake lachinayi pa 28 mwezi uno.

Papayu wati atula pansi undindowu chifukwa choti wakula kotero kuti sangakwanitse kutumikira monga momwe udindowu umafunira.

Polengeza za ganizoli kudzera m'chikalata chomwe likulu la mpingowu latulutsa ,Papayu wati akudziwa bwino kuti udindowu umafuna kudzipereka kwatunthu  kudzera m'mapemphero, kusauka komanso kudzipereka munjira zosiyanasiyana zomwe wati sangathenso kukwanitsa malinga ndi nsinkhu wake.

"Zinthu zikusitha pafupipafupi masiku ano zomwe zikusowa maganizidwe komanso matupi olimba pofalitsa uthenga wabwino pantchito yomwe Petulo Woyera anayisiya m'manja mwa apapa mumpingowu,"watero Papa Benedikito wa 16.

Iye wati miyezi ingapo yapitayi wakhala akulephera kugwira bwino ntchito yake yomwe mpingowu unamukhulupirira nayo.

Papayu watsimikizira anthu kuti watula pansi udindowu mwaufulu wake wonse ndipo wati udindowu udzakhala wopanda munthu kuyambira lachinayi pa 28 mwezi uno nthawi ya 8 koloko madzulo.

Iye wathokoza anthu kamba koonetsa chikondi ndi  kudzipereka munjira zosiyanasiyana panthawi ya utumiki wake  ndipo wapempha anthu kuti amukhululukire pazimene amalakwitsa.

"Ndikuika utsogoleriwu mwa Yesu Khristu kuti ndi thandizo la Amayi Maria, akuluakulu omwe amasankha papa watsopano  akwanitse kusankha ntsogoleri wina", watero papayu.

Papayu wati apitiriza kutumikira mpingowu kudzera m'mapemphero pamene tsopano akupuma.

Papa Benedikito wa 16 anasakhidwa pa 19 epulo 2005.

 

 


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>