Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all 1875 articles
Browse latest View live

Kaliati Wayamikira Mpingo Wakatolika Podzipereka Kufalitsa Uthenga Wabwino

$
0
0

Mpingo wakatolika m’dziko muno awuyamikira kamba kodzipereka pa ntchito zofalitsa uthenga wabwino.

Nduna ya zofalitsa nkhani ndi kuphunzitsa anthu zinthu zosiyanasiyana mayiPatricia Kaliati ndi omwe anena izi ngati mlendo wolemekezeka pa mwambo wokhazikitsa chimbale cha nyimbo zowonera cha kwayayaamayi yaSt. Symon and Jude kuChilekamumzinda waBlantyre.

Iwo ati kudzera mu zomwe amayiwa achita zasonyezelatu kuti mpingowu ukudzipeleka polimbikitsa akhristu ake pa ntchito yofalitsa uthenga wa bwino.

Polankhulanso  m’modzi mwa akuluakulu omwe amayendetsa mwambowo  mayiLucy Vokhiwaanati ndi okondwa kuti kwaya yawo yakwanitsa khumbo lake lotulutsa chimbalechi.

“Tikuthokoza Mulungu kamba koti zimene timafuna zachitika  komanso mgwirizano womwe unalipo  pakati pa amayiwa kuti zonsezi zitheke,” anatero a Vokhiwa.

Mutu wa chimbalechi  ndi wakuti “Mzimu wa Ambuye Utamandike.


Ntchito Yolumikiza Magetsi Mmidzi Idya 8 Billion Kwacha

$
0
0

Boma lati ntchito yolumikiza magetsi m’madera akumidzi ikuyembekezeka kudya ndalama zokwana 8 Billion kwacha.

Nduna yoona za chilengedwe komanso mphamvu za magetsi a Bright Nsaka ati gawoli ndi la nambala 8 ndipo unduna wawo uyesetsa kuti anthu mdziko muno maka m’madera akumidzi akhale ndi mwayi okhala ndi magetsi.

Iwo amalankhula izi lolemba lapitali mu mzinda wa Blantyre pomwe amalandira katundu wina othandizira pa ntchitoyi kuchokera ku  Cullin Africa.

Ntchitoyi ikuyembekezeka kufikiranso zipatala zina potsatira zomwe phungu wa kunyumba ya malamulo wadera la kumvuma kwa boma la Dedza adapempha posachedwapa m’nyumba ya Malamulo.

Mphamvu za Mpingo Wakatolika Zili pa Akhristu Ovutika Mchikhulupiliro-Papa

$
0
0

Mtsogoleri wa mpingo wa Katolika pa dziko lonse Papa Fransisko wati mphamvu za mpingo wa Katolika zatsamira kwambiri pa akhristu ochepa omwe akuvutikabe kaamba ka chikhulupiliro chawo.

Iye amalankhula izi pa mwambo wa nsembe ya Misa KU Tchalitchi cha Casa Santa Martha lolemba lapitali.

Papa Francis wati maziko a mpinguwu sanagone pakungoyankhula chabe koma pa akhristu okhazikika pa chikhulupiliro chawo.

Malinga ndi Papa Francisko mphamvu za mpingowu zagona pa mipingo ing’onoing’ono, yopezeka ndi anthu ochepa ndipo maepiskopi ake ena ali m’ndende kaamba kachikhulupiliro chawo.

Dayosizi ya Mangochi Ilimbikitsa Achinyamata Kutenga Mbali mu Mpingo

$
0
0

Dayosizi ya mpingo wa katolika ya Mangochi yati iwonetsetsa kuti achinyamata akutenga nawo mbali pa zochitika zonse za mpingo.

Mlembi wa episkopi wa dayosiziyi bambo Steven Kamanga anena izi pa msonkhano wokhazikitsa bungwe latsopano loyang'anira achinyamata mu dayosiziyi lomwe akulitcha Youth Animation Team (YAT).

Iwo ati dayosiziyi yakonza dongosolo loti achinyamata azipezeka mu zochitika zilizonse za mpingo ndi cholinga choti agwilire ntchito limodzi kuti mapulani a dayosiziyi okweza achinyamata apite patsogolo.

Polankhulapo mkulu wa kuofesi yoona za achinyamata mu dayosiziyi, bambo Christopher Sichinga ati kubwera kwa gululi kuthandiza kuti ntchito zina za achinyamata zomwe zimavuta ziyambe kuyenda bwino.

Iwo ati ngakhale m’chaka cha 2016 akumana ndi zovuta zina koma chaka chino ayesetsa kuti akwaniritse zolinga zawo zonse zomwe akonza.

Dziko La Indonesia Lidzudzula President Trump

$
0
0

Wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko la Indonesia a Jusuf Kalla wati ndondomeko yomwe dziko la America lokonza poletsa anthu ochokera ku Mayiko a chisilamu kulowa mdziko la America, kukupereka chikayiko pa m’mene dzikolo likuwaganizira asilamu.

A Kalla ati ndondomekoyo silingakhudze kwambiri dziko lawo koma likupereka chikayiko pa m’mene dziko la America likuganizira asilamu.

Dziko la Indonesia ndi limodzi mwa mayiko omwe kuli asilamu ambiri koma silili pa m’ndandanda wa mayiko omwe anthu ake awaletsa kulowa mdziko la America.

A Donald Trump alamula kuti anthu ochokera m’mayiko achisilamu monga Syria, Iran, IRAQ, Libia, komaso Sudan asamalowe mdziko la America.

Trump wati Sakudana ndi Chipembedzo cha Chisilamu

$
0
0

Mtsogoleri wa dziko la America Donald Trump wati ganizo lake loletsa nzika zina zochokera ku mayiko ena achisilamu kulowa mdzikolo sikukutanthauza kuti akudana ndi chipembedzo chachisilamu.

A Trump alankhula izi pomwe mzika zina za mdziko la America komanso mayiko ena akhala akuchita ziwonetsero zosagwilizana ndi ganizo la boma la America-lo.

Iwo ati dziko la America limasangalala ndi anthu a m’mayiko ena ndipo lipitiliza kuwalemekeza komabe kwinaku likuteteza mzika zake ku malire a dzikolo.

Anthu mazanamazana akhala akuchita ziwonetsero m’mizinda ya dzikolo posagwilizana ndi ganizolo ndipo ambiri akudandaula kuti dzikolo likuchita tsankho.

Papa wati Chipulumutso Chikuyenera Kuvalidwa Ngati Chipewa

$
0
0

Mtsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Francisco wapempha akhristu kuti avale chiyembekezo cha chipulumutso ngati chipewa chodzitetezera pa ngozi ya njinga  pozindikira kuti kuwuka kwa khristu kumapherezera chiyembekezocho.

Papa amalankhula izi pa mkumano omwe anali nawo ndi anthu ochokera mmadera osiyanasiyana omwe anakayendera likulu la mpingo wakatolikali ku Vatican mu mzinda wa Rome mdziko la Italy.

Papa wati chiyembekezo cha chikhristu, ndi kudikira chinthu chimene chakwaniritsidwa kale zomwe aliyense akuyenera kuzindikira monga momwe mayi amachitira akazindikira kuti ndi woyembekezera, amadikira tsiku ndi tsiku mphatso ya mwana.

Pamenepa Papa wati Paulo woyera analemba kuti ‘Yesu khristu anafera aliyense kuti pa nthawi imene aliyense wagona kapena kudzuka azikhala naye limodzi’ omwe ndi mau a chitonthozo komanso mtendere. 

Pomaliza Papa anapempha akhristuwa kuti apitirize kupanga maubale ndi cholinga choti mpingo upitirize kutengapo gawo pa anthu osawuka ngakhalenso pa zomwe zikuchitika pa dziko lonse.

Mamuna Wina Wamira M’boma la Ntchisi

$
0
0

Mamuna wina m’boma la Ntchisi ati wafa atamira mu mtsinje wa Bua komwe anapita kukawedza nsomba.

Wofalitsa nkhani za apolisi mbomali Sergent Gladson M’bumpha watsimikiza za nkhaniyi.

Sergent M’bumpha wati mamunayu Samson Yola wa zaka 31 zakubadwa yemwe amadwala matenda a khunyu anapita kokawedzaku ndi mng’ono wake Gaison Yola yemwe anasiya malemuyu ndi kubwelera kunyumba.

Malipoti ati malemuyu sanabwelere kunyumba usiku onse zomwe zinachititsa kuti tsiku lotsatira bambo ake ndi anthu ena ayambe kumuyang’ana pomwe anakamupeza ku mtsinjeki atamira.

Sergent M’bumpha ati akuganizira kuti malemuyu anagwidwa ndi matendawa pa nthawi yomwe amawedza zomwe zinachititsa kuti agwere mu mtsinjemo.

Malipoti a ku chipatala chaching’ono cha Malomo m’bomalo asonyeza kuti malemuyu wafa kamba koti amalephera kupuma.

Malemuyi ankachokera mmudzi mwa Khasu kwa mfumu yaikulu Chilooko m’boma lomwelo la Ntchisi.


Papa Francisko Wakhazikitsa Stanislaus ndi Maria Elizabeti Kukhala Oyera

$
0
0

Mtsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Francisko wakhazikitsa Stanislaus wa Yosefe ndi Maria komanso Maria Elizabeti Hesselblad kukhala oyera.

Papa wakhazikitsa awiriwa kukhala oyera lamulungu pa mwambo wa nsembe ya misa ku likulu la mpingowu ku Vatican.

Papa anayamikira  awiriwa kamba ka chikhulupiliro chomwe anali nacho komanso kupilira kwao pa nthawi yomwe anali kukumana ndi mayesero.

Iye wati kudzera mu mazunzo a yesu awiriwa anali okhudzidwa ndipo zinachititsa kuti chinsinsi cha mphamvu ya kuuka kwake chiwululike mwa iwo.

Pa mwambowu panafika nthumwi za mmaiko a Sweden ndi Poland komwe oyerawa ankachokera.

Anthu Asanu Ochita Masewero Opalasa Njinga Afa Atagundidwa Ndi Galimoto

$
0
0

Anthu asanu ochita masewero opalasa njinga afa ndipo ena anayi avulala galimoto lina litawaomba ku Michigan m’dziko la America.

Anthu-wa ati agundidwa ndi galimoto la mtundu wa Pick Up lomwe pa nthawiyo limayenda mu msewu umene anthuwo amagwilitsa ntchito pochita masewerawo.

Malinga ndi malipoti a wailesi ya BBC apolisi m’dzikolo ati agwira dalaivala yemwe amayendetsa galimotolo yemwe pa nthawi ya ngoziyo akuti anathawa.

Padakali pano anthu omwe avulalawo akulandira thandizo ku chipatala china mu m’dzikomo

 

Papa Apempha Akhristu Azipemphelera Atumiki a Mulungu

$
0
0
Mtsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Francisco wapempha anthu kuti azipemphelera atumiki a Mulungu omwe anayitanidwa kuti atumikire Mulungu. Papa amalankhula izi ku likulu la mpingowu ku Vatican pomwe lero mpingo ukuchita chaka cha kuperekedwa kwa Ambuye yesu mu tempile lomwenso ndi tsiku loganizira atumiki a Mulungu. Iye wati akhristu akuyenera kupemphelera ansembe, asisteri, ablazala a mzipani zosiyanasiyana kuti kudzipereka kwao potumikira Mulungu kubale zipatso zabwino mwa anthu okhulupilira komanso kuti cholinga cha mpingo chikwaniritsidwe. Pamenepa Papa wapempha atumiki a Mulunguwa kuti azipemphera mozama ndi cholinga choti afalitse chikondi cha khristu komanso chaulele cha mthenga wabwino.

Ambuye Msusa Adandaula Kamba ka Kusagwiritsa Ntchito Bwino Chilengedwe

$
0
0

Arkiepiskopi wa arkidayosizi ya Blantyre ya mpingo wakatolika Ambuye Thomas Luke Msusa wadandaula kuti dziko la Malawi likulephera kugwiritsa  ntchito moyenera zachilengedwe zomwe lili nazo.

Ambuye Msusa amalankhula izi ku Bingu International Conference Centre mu mzinda wa Lilongwe pa mwambo wopereka ma Degree kwa ophunzira 161 omwe atsiriza maphunziro awo ku sukulu ya ukachenjede ya DMI St. John the Baptist.

Iwo apempha ophunzirawa kuti adzetse kusintha pobweretsa zinthu zoyenera zomwe zingathandize kutukula dziko lino ngakhalenso miyoyo ya anthu.

Msilikali Amangidwa Kamba Kobera Anthu Ndalama

$
0
0

Apolisi m’boma la Karonga ati akusunga mchitokosi msilikali wina wa ku Cobbe barracks ku Zomba kaamba komuganizira kuti amalandira ndalama zokwana 80 sauzande kwacha kwa anthu a mmidzi ina ya m’bomalo ndi cholinga choti awapezere ntchito ya usilikali anthuwo.

Wachiwiri kwa ofalitsa nkhani za apolisi m’bomalo Constable Davie Mulewa wauza Radio Maria Malawi kuti msilikaliyu Loti Mwakisulu wa zaka 27 zakubadwa wa mmudzi mwa Mwakisulu kwa mfumu yaikulu Kilupula m’bomalo wakhala akuchita izi kuyambira chaka chatha kwa anthu omwe anamaliza sukulu yao kufika fomu 4.

Iwo ati apolisi akhala akumva za mphekesera ya mchitidwewu kufikira dzulo pomwe anatsinidwa khutu ndi anthu a mmudzi wa Mwakawoko m’bomalo komwe msilikaliyu anafika pa nthawiyo.

Apolisi M’dziko la New Guinea Akuwaganizira Kuti Apha Ophunzira Anayi Omwe Amachita Chionetsero

$
0
0

Apolisi m’dziko la New Guinea akuwaganizira kuti apha ophunzira anayi   a pa sukulu ina ya ukachenjede omwe amachita chionetsero chosonyeza kusakondwa ndi zochita za nduna yaikulu ya dzikolo.

Malingana ndi malipoti a wailesi ya BBC chionetserocho chinayambira ku sukulu yawo ndipo chinakathera ku nyumba yamalamulo ya dzikolo.

Ophunzira-wa ati akufuna kuti ndunayi itule pansi udindo wake kuti ikayankhe milandu ya ziphuphu ndi katangale.

Malipoti ati ndunayi ikukana kutula pansi udindo wake ndipo yati sikudziwapo kanthu pa nkhanizi.

Anthu Makumi Atatu Afa Zigawenga za Islamic State Zitaphulitsa Bomba La Timke Nawo

$
0
0

Anthu makumi atatu afa, ndipo ena 80 avulala  gulu la zigawenga la Islamic State litaphulitsa  mabomba awiri atinkenawo  munzinda wa Baghdad  m`dziko la Iraq

Malinga ndi malipoti awailesi ya BBC, bomba loyamba linaphulika m`dera la Shiandipo linapha anthu 19 pomwe bomba lina linaphulika  pamalo ena pomwe asilikali amachitira chipikisheni  a Taji kumpoto kwa mzinda wa Baghdad  ndikupha  anthu  11 kuphatikizapo asilikali.

Gulu la zigawengazi ati likupitiriza kuchita zamtopola  munzindawu pomwe asilikali adzikoli akulimbikitsa  ntchito  yolanda   maziko azigawengazi otchedwa  Falluja  omwe ali pamtunda wa makulomita 60 kumwera kwa mzinda wa Baghdad.


Anthu Asanu Ochita Masewero Opalasa Njinga Afa Atagundidwa Ndi Galimoto

$
0
0

Anthu asanu ochita masewero opalasa njinga afa ndipo ena anayi avulala galimoto lina litawaomba ku Michigan m’dziko la America.

Anthu-wa ati agundidwa ndi galimoto la mtundu wa Pick Up lomwe pa nthawiyo limayenda mu msewu umene anthuwo amagwilitsa ntchito pochita masewerawo.

Malinga ndi malipoti a wailesi ya BBC apolisi m’dzikolo ati agwira dalaivala yemwe amayendetsa galimotolo yemwe pa nthawi ya ngoziyo akuti anathawa.

Padakali pano anthu omwe avulalawo akulandira thandizo ku chipatala china mu m’dzikomo

 

Papa Wati Akhristu Apempherere Mtendere wa Mmaiko Onse

$
0
0

M’tsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Franciskowapempha anthu ndi akhristu a mpingowu kuti lachitatu akumbukire kupemphelera mtendere wa m’mayiko pa dziko lonse.

Malinga ndi malipoti a nyuzipepala ina ya mpingowu, Papa wati wachita izi pomwe mpingowu ukukumbukira kuti patha zaka ziwiri chikhazikitsireni m’gwilizano wa pakati pa atsogoleri a mpingowu ndi a maiko a Israel ndi Palestine opemphelera mtendere m’maiko a Aluya.

Malipoti ati mapemphero a chaka chino, anthu akuyenera kulimbikitsa mapemphero pakati pa anthu omwe akuthawa m’maiko awo kamba kosowa ntchito komanso nkhondo kuti azindikire za chikondi choposera chomwe Mulungu amakhala nacho pakati pawo.

Nthambi Ya Zachilungamo Igwirizana Ndi Lamulo La Trump

$
0
0

Nthambi ya zachilungamo mdziko la America yati ikugwirizana ndi zomwe mtsogoleri wa dzikolo, Donald Trump wachita poletsa  anthu a m’maiko ena a chisilamu kolowa mdzikolo.

Malinga ndi malipoti a wailesi ya BBC,  nthambiyi yati presidentiyu wachita izi kudzera mu mphamvu zomwe amapatsidwa kuchokera m’malamulo oyendetsera dzikolo ndipo  apempha bwalo lalikulu la milandu mdzikolo kuti lamuloli liyambe kugwira lipitilire kugwira ntchito poganizira chitetezo cha dzikolo.

Lamuloli likuletsa anthu othawa kwawo komanso alendo ochokera m’maiko asanu ndi awiri omwe ndi a chipembedzo cha chisilamu kulowa mdziko la America.

Bwalo lalikulu la milandu la dzikolo likuyembekezeka kupereka chigamulo chake lero kuti lamuloli lipitilire kugwira ntchito kapena ayi.

Pakadali pano anthu a m’maiko asanu ndi awiriwa 7, Iraq, Iran, Libya, Somalia, Sudan, Syria komanso Yemen omwe ali ndi zitupa zoyenera akupitilirabe kulowa mdzikolo.

Mayi Afa pa Ngozi ya pa Nsewu M’boma la Mangochi

$
0
0

Mayi wina wa zaka 52 zakubadwa wafa atawombedwa ndi galimoto m’boma la Mangochi.

Wofalitsa nkhani za apolisi m’bomalo Sergeant Amina Tepani Daudi wauza Radio Maria Malawi kuti mayiyu Martha Kuswenje anawombedwa ndi galimoto ya mtundu wa Rav4 nambala yake BT 9292 yomwe imayendetsedwa ndi a Ganet Fologonya a zaka 51 a m’mudzi mwa James mfumu yaikulu Kuntaja m’boma la Blantyre.

Sergeant Daudi ati galimotoli lomwe limalowera ku Namwera linali pa liwiro lamphamvu ndipo litafika pa round about ya pa St. Augustine Mangochi Cathedral dalaivala analephera kuwongolera bwino ndipo inaphonya nsewu ndi kugubuduka kangapo ndi kukawomba mayiyu yemwe amayenda m’mbali mwa nsewuwu. Mayiyu ati anavulala kwambiri ndi kufera pomwepo.

Pakadali pano apolisi m’bomali achenjeza anthu kuti azitsatira malamulo a pansewu kuti apewe ngozi za mtunduwu.

Mayi Martha Kuswenje amachokera m’mudzi mwa Chipalamawamba mfumu yaikulu Mponda mboma lomwelo la Mangochi.

Kanyongolo Wapempha Boma Libwezeretse Maubale Ndi Maiko Ena

$
0
0

Katswiri wa malamulo yemwenso ndi mphunzitsi wa malamulo pa sukulu ya ukachenjende ya Chancellor, Professor Edge Kanyongolo wapempha boma  kuti libwezeretse ubale womwe unasokonekera pakati pa boma la Malawi ndi mayiko komanso mabungwe omwe amathandiza  dziko lino pa chuma.

Professor Kanyongolo wanena izi lachinayi poyankhula  ndi Radio Maria Malawi .

Iwo ati ndondomeko yachuma yachaka chino ipweteketsa anthu osauka chifukwa adzidulidwa nsonkho akagula katundu  wina aliyense.

A Kanyongolo ati dziko la Malawi silinafike podzidalira palokha pachuma chifukwa lilibe zinthu zoziyenereza monga migodi ndi makampani akulu akulu. Iwo ati dziko la Malawi limadalira fodya yekha pa chuma yemwenso sakuyenda bwino pa msika.

Kaswiri wa malamulo-yi wati boma liyenera kuvomereza kuti zinthu mdziko muno sidzilibwino pa chuma. Iwo ati zipatala za mdziko muno muli mavuto ambiri  monga kusowa mankhwala komanso kuchepa kwa ogwira ntchito ndipo wati izi zikusonyeza kuti boma lili pa mpanipani wosonyeza kuti lilibe chuma choyendetsera dziko.

Pa nkhani ya njala yomwe ili m’dziko muno Professor Kanyongolo wapempha boma kuti ligule chimanga chambiri kuti chizakwanire anthu onse omwe alibe chokudya. Iwo ati boma lisadzalowetse ndale podzagawa chimangachi koma chidzafikire aliyense.

Viewing all 1875 articles
Browse latest View live


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>