Ophunzira pa sukulu ya ukachenjede ya Chancellor ati apitiliza kunyanyala maphunziro awo pokhapokha akulu-akulu a mu khonsolo yowona za maphunziro pa sukulu-yi (University Council) atabwera ndi maganizo otsitsa mtengo wa suluku fiziya ophunzira pa sukulu-yi.
M’tsogoleri wa ophunzira-wa Eunice James wanena izi pofotokozera Radio Maria Malawi amene amafuna kudziwa zambiri zokhudza nkhani ya kunyanyala kwa maphunziro komwe ophunzirawa akuchita pa sukuluyi.
Iye wati ophunzira pa sukulu-yi sasiya kuchita zionetsero zi kufikira akulu-akulu-wa, atamvera maganizo awo ndi kutsitsa mtengo watsopano wa ndalama za sukulu zolipilira maphunziro a pa sukulu-yi.