Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

MUM Iyamikira Boma Podutsitsa Bilu ya Copyright

$
0
0

Bungwe la anthu oyimba mdziko muno la Musicians Union Of Malawi (MUM) layamikira boma podutsitsa bilu yoteteza luso la anthu oyimba ya Copyrightkunyumba ya malamulo.

Wapampando wa bungweli mdziko muno a Chimwemwe Mhango ndi omwe anena izi polankhula ndi Radio Maria Malawi.

Iwo ati biloyi yomwe ikukakamiza munthu wopezeka akubera nyimbo kulipira ndalama zokwana 10 million kwacha kapena kukakhala ku ndende kwa zaka zinayi, ithandiza kutukula miyoyo ya anthu aluso mdziko muno.

“M’mbuyomu timafuna kuyenda munsewu ngati oyimba kuti tisonyeze kukwiya kwathu chifukwa bilu yathu simalowa mu parliament ndipo anduna anatitsimikizira kuti zitheka. Anachitadi zothekera mpaka bilu ija yalowadi mu parliament. Ndife osangalala kwambiri ngati oyimba chifukwa boma kudzera mwa anduna lamva kulira komanso madandaulo athu. Zimenezi zikusonyeza kuti ndi boma lakumva kulira komanso madandaulo a anthu. Ndife onyadira tsopano kuti biluyi yadutsa ku nyumba ya malamulo.

Vuto lalikulu lomwe tilinalo ndi mchitidwe woberana luso. Anthu sakulemekeza luso la anzawo akungobena nyimbo mwachisawawa kumagulitsa mkumapeza ndalama pamene mwini wake anakhetsa thukutayo akuvutika. Biluyi ithandiza kuti mchitidwe umenewu uchepe ndipo pamapeto pake miyoyo ya oyimba ndi aluso itukuka, tiyamba kupindula pa luso lathu,” anatero a Mhango.

A Mhango achenjeza anthu onse akubena nyimbo mmadera osiyanasiyana kuti alekeretu mchitidwewu kamba koti biluyi ikakhazikitsidwa lamulo ligwira ntchito pa iwo.

“Ndichenjeze anthu amene akhala akutibera nyimbo ndi makina awo kuti nthawi yakwana, tiyeni tisiye, tikapanda kutero tikavutika kundende nthawi yaitali,” anatero a Mhango.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>