Bungwe la maepiskopi a mpingo wakatolika mdziko la Philippines la Catholic Bishops Conference of the Philippines ladzudzula apolisi mdzikolo kamba ka mchitidwe wakupha anthu a mdzikolo omwe akuwaganizira milandu yosiyanasiyana.
Malinga ndi kalata yomwe bungweli latulutsa maepiskopiwa ndi okhudzidwa ndi kukwera kwa chiwerengero cha anthu omwe akuphedwa kaamba kopalamula milandu yosiyanasiyana mdzikolo ati kaamba koti akumakana kumangidwa.
Kalatayi yati ngakhale zili zololedwa kupha munthu pofuna kudziteteza, apolisiwa sakuyenera kupha anthu oganiziridwa kaamba kofuna kulandira ndalama.