Mtsogoleri wa mpingo wa katolika pa dziko lonse papa Francisco anatsogolera mwambo wokumbukira anthu oposera 1.1million omwe adafa mdziko la Poland.
Malinga ndi malipoti a wailesi ya BBC, Papa atafika pamalo anapempha anthu kuti akhale chete kwa mphindi zingapo pokumbukira anthuwa komanso, anapemphera pemphero lapadera lopempherera mizimu ya anthuwo, omwe ambiri mwa iwo anali a Yuda.
Mwa zina papa anaimanso pa ndende ya Maximilian Kolbe, amene mpingo unamutcha oyera mchaka cha 1982, ndipo pamolopa papa anayatsapo kendulo ndikupemphera atagwada kwa mphindi zochuluka.
Papa anafika mdzikolo pa 27 mwezi uno pa ulendo wake wa masiku asanu wokacheza, patatha zaka chikwi chimodzi ndi makumi asanu chiyambire chi khristu mdzikolo.