Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Anthu 6.5 Million Ayamba Kulandira Chakudya

$
0
0

Anthu pafupifupi 6.5 million omwe akhudzidwa ndi vuto njala mdziko muno ati apindula ndi thandizo la chakudya lomwe boma kudzera ku bungwe lowona za chakudya pa dziko lonse la World Food Programme mothandizana ndi mabungwe omwe si aboma apereke.

Malinga ndi uthenga omwe mlembi mu ofesi ya wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino a Ben Botolo atulutsa, zotsatira za kafukufuku wa komiti ya Malawi Vulnerability Assessment (MVAC) linachita, anthu pafupifupi 6.5 million akusoweka thandizo la chakudya kuyambira mmwezi wa July chaka chino mpaka mmwezi wa March chaka cha mawa.

Bungwe la WFP lati lithandiza anthu 5.85 million ndipo ena 650 sauzande athandizidwa ndi mabungwe omwe si aboma.

Wachiwiri wa mtsogoleri wa dziko lino, Dr. Saulos Klaus Chilima ndi yemwe watsegulira mwambo woyamba kugawa chakudyawu mdziko muno pa sukulu ya pulaimale ya Nyamitalala kwa mfumu yaikulu Mbenje m’boma la Nsanje lomwe ndi boma limodzi lomwe lakhudzidwa kwambiri ndi vuto la njala mdziko muno.

Iwo apempha mabungwe, mipingo komanso anthu akufuna kwabwino kuti agwirane manja ndi boma pothandiza anthu amene akhudzidwa ndi njala mdziko muno.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>