Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Mpingo Wakatolika Mdziko Muno ati Udzapindula ndi Msokhano wa WUCWO

$
0
0

Mpingo wakatolika mdziko muno akuti udzapindula kwambiri ndi msonkhano wa bungwe la amayi achikatolika pa dziko lonse waWorld Union of Catholic Women Organisation(WUCWO)umene awukonza kuti uchitikire m’dziko muno chaka chino.

Wachiwiri kwa wapampando wa komiti yoyendetsa dongosolo la msonkhano-wu m’dziko muno mayiAnita Kaliwuanena izi pomwe amafotokozera atolankhani ochokera mu nyumba zofalitsa nkhani za mpingo wakatolika amene akuchita msonkhano wawo m’boma la Salima.

Iwo ati mfundo zomwe amayi adzakambilane ku msonkhanowu zizathandizanso kwambiri pa chitukuko cha dziko lino.

“Tikhala ngati tikugulitsa dziko lathu alidziwe komanso ndi zimene tikuchita kuno ku Malawi. Zithandiza kulimbikitsa amayi komanso kugawana mavuto amene tili nawo ofanana m’maiko athu ndikugawana njira zothetsera mavutowo. Mavuto monga a kusintha kwanyengo akukhudza maiko ambiri muno mu Africa ndiye tikakambiarana tipeza njira zochepetsa kapena kuthetselatu mavuto amenewa,” anatero mayi Kaliwu.

Msonkhano wa bungwe la amayi achikatolika pa dziko lonse laWorld Union of Catholic Women Organisation(WUCWO)udzasonkhanitsa amayi a mbungweli ochokera m’mayiko 22 a muno mu Africa ndipo udzayamba pa 30 mwezi uno, ndi kutha pa 6 September mu m’dzinda waLilongwe.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>