Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

PAC Ikuphunzitsa Amayi Luso Lobweretsa Mtendere

$
0
0

Bungwe la mgwilizano wa mipingo ndi zipembedzo laPublic Affairs Committee(PAC)lati likufuna kulimbikitsa kuphunzitsa amayi luso lothandiza kubweletsa mtendere pa nkhani zosiyanasiyana zochitika m’dziko muno.

Wapampando wa bungwelim’busaDr. Felix Chingotawalankhula izi potsekulira maphunziro a amayi ochokera m’mipingo yosiyanasiyana yomwe ili pansi pa bungweli.

Dr. Chingota ati amayi ali ndi kuthekera kobweletsa mtendere m’dziko kotero kuti akuyenera kulimbikitsidwa pa ntchito-yi.

“Pamene tikutukula dziko lino PAC imawonanso kuti ndi pofunika kuti amayinso nawo atengepo gawo. Amayi tikufuna kuwagwiritsa ntchito ngati zida zodzetsa mtendere pamene pali kusamvana,” anatero Dr. Chingota.

Mlembi wa mkulu wa bungwe la amai ochokera mu mipingo ndi zipembezo zosiyanasiyana m’dziko muno mayi Agness Kamoto anati zimenezi zithandizira kuti mavuto ena amene amakhala mdziko muno asapite patali.

“Munthu wa mayi ndi amene amamvetsera zinthu bwino komanso amamvetsetsa. Choncho amayi tikatengapo mbali pa mavuto ena amene amakhala mdziko muno tipanga Malawi wa bata ndi mtendere,” anatero mayi Kamoto.                                             


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>