Bungwe la Angoni omwe akupezeka mu mzinda wa Blantyre la Maseko Ngoni Blantyre Chapter lapempha anthu kuti agwirane nawo manja pothandizapo pa mavuto omwe odwala a pachipatala cha Ntcheu amakumana nawo.
Wapampando wa bungweli a Chauluka Dimba ndi omwe apereka pempholi pambuyo pa ulendo wa ndawala omwe bungwe lawo linayenda mu mzinda wa Blantyre ndi cholinga chofuna kutolera thandizo lokapereka kwa odwala a pa chipatala cha Ntcheu.
Iwo ati kupatula odwala, ogwira ntchito nawo akusowa zipangizo zina zowathandiza kugwira bwino ntchito yawo.
“Tawona kuti anzathu kuchipatala cha Ntcheu akusoweka thandizo zomwe patokha sitingakwanitse choncho tikupempha anthu akufuna kwabwino atithandize kuti mavuto amenewa achepe. Odwala amene ali kumeneku si angoni okha koma ndi amitundu yonse chonse aliyense atengepo gawo,” anatero a Dimba.
Iwo ati ndalama yomwe ikufunika ndiyokwana 20 million yoti ithandizire odwalawa komanso ogwira ntchito pa chipatalachi kuti nchito zawo za tsiku ndi tsiku ziyende bwino.