Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Jacobs Mwase 'Zakaliya' Wamwalira

$
0
0

M'modzi mwa akatswiri a zisudzo mdziko muno Jacobs Mwase amene amatchukandi dzina loti a Zakaliya wamwalira.

M'modzi mwa akuluakulu omwe amachita zisudzo mugulu la Kwathu Drama, a Eric Mabedi atsimikiza za nkhaniyi.

A Mabedi ati Mwase wamwalira lero (lachitatu) m'mawa ku chipatala chachikulu cha boma la Thyolo.

Padakali pano anthu azisudzo mdziko muno ati ndi okhudzidwa kwambiri ndi imfayi poganiziranso kuti pangotha miyezi itatu chimwalilireni a John Nyanga yemwe amatchuka ndi dzina loti Izeck yemwe amachitanso zisudzo.

"Tataya munthu ofunikira kwambiri ndipo kwa ife ndi zovuta kwambiri chifukwa pangotha miyezi itatu yeniyeni chimwalilireni John Nyanga. Ife a Kwathu Drama Group tinayimikira marehearsal athu kuti pathe miyezi itatu chimwalilireni a Nyanga moti timayembekezeka kuyambanso ma rehearsal athu mu September muno ndi pamene zikuchitikanso izi. Ndiye poti zachitika kale nanga titani. amene akumwalirawa ndi a mkhalakale pa zisudzo okhaokha palibe amene wayamba dzana ayi. Ndi anthu oti ofunikira kwa ife azisudzo, ku banja komanso a Malawi onse monga mudziwa amachitanso sewero lija la Sabata ino pa Radio 1," anatero a Mabedi.

A Mabedi ayamikira luso lalikulu lomwe a Mwase anali nalo kumbali ya zisudzo mdziko muno ndipo iwo apitiriza ponena kuti anthu azisudzo mdziko muno adzalisowa luso la a Mwase. Iwo ati a Mwase achita mbali yaikulu ku mbali ya zisudzo ndipo anati ndi munthu wamkulu yemwe sanalembedwepo ntchito ndi kampani iliyonse koma amalimbika kwambiri pa luso lake.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>