Anthu otsutsa boma zikwizikwi mu mzinda wa Caracasm’dziko la Venezuela ati anachita zionetsero pofuna kuti mtsogoleri wa dzikolo Nicholas Maduro achotsedwe pa udindo wake.
Malinga ndi malipoti a wailesi ya BBC, anthuwa anachita izi ati kaamba koti Pulezidenti Maduro ndi yemwe akuchititsa kuti dzikolo likhale pa mavuto a zachuma komanso kuti bungwe lowona za chisankho m’dzikolo lichedwetse chisankho chofuna kumva maganizo a anthu zomwe zingachepetse nthawi yokhala pulezidentiyu pa ulamiliro.
Malipoti ati anthu otsatira pulezidentiyu anachita msonkhano ati ponena kuti anthu otsutsa bomawa akungofuna kuchita zamtopola.