Akhristu a mpingo wakatolika mdziko muno awapempha kuti agule baibulo la tsopano la mpingowu lomwe akulitcha New Catholic Answer Bible ndi cholinga choti azame mu chikhulupiliro chawo komanso chiphunzitso cha mpingowu.
Wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino Dr. Saulos Chilima wapereka pempholi ku tchalitchi la St. Louis Montfort (CI) parish mu archdayosizi ya Blantyre.
Iwo ati baibulo latsopanoli likuthandiza akhristu kuyankha mafunso ambiri omwe akhristu ampingo wakatolika amakumana nawo omwe amasowa mayankho ake.
“M’chaka cha 2012 achinyamata asukulu atapita ku msonkhano anawonetsa kuti pali zina zoperewera zimene samakwanitsa kumvetsa bwino kuti akhoza kumayankha mokwanira zokhudzana ndi chipembedzo cha chikatolika; zina zimene timapanga pa nthawi ya misa komanso miyambo yosiyanasiyana ya mu mpingo wathu wa Eklezia katolika.
Akuluakulu atafufuza anapeza kuti pali mafunso okwana 88 omwe amafunsidwa kawirikawiri kwa akhristu a mpingo wakatolika. Ndipo anawona cha nzeru kuti apezere mayankho ake kuchokera m’baibulo kutanthauza kuti si nkhambakamwa chabe koma ndizaumboni kuti miyambo yomwe timachita akatolika ndiyochoka mbaibulo, sitinangozipeka,” anatero Chilima.
A Chilima anati baibulo latsopanoli silobwerekana ndipo apempha akhristu kuti aliyense akhale nalo lake kaamba koti chikhulupiliro sagawana.
“Baibulo limeneli lili ngati kolona; samabwerekana. Palibe amati ndimafuna ndipemphere ndibwerekeni kolona wanu ayi. Chikhulupiliro sabwerekana aliyense chimakhala chake. Tiyeni tigule kuti tiwone kuti chikhulupiliro cha katolika ndi chani kuti anthu akatifunsa tiziyankha mwamphamvu, momveka komanso molimba mtima kupanga defend chikhulupiliro chathu cha chikatolika,” anatero a Chilima.
Iwo ati baibulo latsopanoli ndi chida chimene chithandize akhristu a mpingo wakatolika kuyankha mwamphamvu mafunso amene amafunsidwa kawirikawiri.