Chiwerengero cha anthu omwe afa pa ngozi yomwe yachitikadzulopa Shoprite mu msewu wa Masauko-Chipembere mu mzinda wa Blantyreakuti chafika pa atatu.
Ngoziyi yachitika dzuro cha ku m’mawa, galimoto la mtundu wa lole lomwe anthu-wa omwe ati ndi mamembala akwaya ya mpingo wa CCAP anakwera, litaphonya msewu ndi kukagwera ku mbari ina ya msewu-wu.
Mamemala akwayawa akuti amachokera ku Luchenza m’boma la Thyolo kupita ku HHI kukachita nawo kwaya festival ya mpingo-wu.
Malinga ndi m’modzi mwa akuluakulu a Blantyre Synod ya mpingo wa CCAP, m’busa Moyenda Kanjerwa, anthu atatu omwe amwalira pa ngoziyi ndi a Christina Chitekwe omwe anafera pa malo angoziwo, a Anastanzia Mendulo komanso a Robert Ntopwa omwe amwalira akulandira thandizo la kuchipatala.