Episikopi wa diyosizi ya Mangochi ya Mpingo wa Katolika Ambuye Allesandro Pagani ayamikira ubale umene ulipo pakati pa diyosiziyi ndi diyosizi ya Bergamo m’dziko la Itary.
Ambuye Pagani alakhula izi lolemba pamene Ambuye Francesco Beschi a diyosizi ya Bergamo anayendera nyumba yofalutsira mawu ku Radio Maria Malawi m’boma la Mangochi.
Iwo ati amakhala okondwa nthawi zonse kamba koti dayosizi ya Bergamo imakhala ikuchita zinthu zosiyanasiyana zolimbikitsa ansembe ndi atumiki ena mu diyosiziyi yawo ya Mangochi maka omwe akutumikira m’chipani cha Mofolo woyera.
“Dayosizi ya Bergamo ikuthandiza kwambiri ansembe athu kuno ku dayosizi yathu ya Mangochi,maka kwa iwo omwe akutumikira kuno ku Malawi kuchokera ku Italy”, atero Ambuye Pagani.
Ambuye Beschi anayenderanso nyumba yosindikiza nkhani ya Montifort Media ku Balaka komwe athandiza ndi makina a makono osindikizira mabuku a ndalama zoposa 50 miliyoni kwacha.
Ambuye Beschi akuyembekezekanso kuyendera malo osiyasiyana mu diyosizi ya Mangochi.