Bungwe la ma episkopi a mpingo wakatolika mdziko muno la Episcopal Conference of Malawi ECMlalengeza kuti lasankha bambo Regis Kamela kukhala wansembe woona za utumiki ku bungweli.
Malinga ndi kalata yomwe bungweli latulutsa yomwe yasayinidwa ndi mlembi wamkulu wa bungweli bambo Henry Saindi, bungweli linasankha bambowa pa udindowu omwe wakhala ukugwiriziridwa ndi Bambo Vincent Mwakhwawa pa msonkhano waukulu wachiwiri wa maepiskopi wa chaka chino omwe linali nawokuyambira pa 27 June kufikira pa 1 July.
Kalatayi yati malinga ndi malamulo a bungweli bambowa akhalanso wachiwiri kwa mlembi wamkulu wa bungweli.
Bambo Kamela anadzozedwa kukhala wansembe mu chaka cha 1988, ndipo kufikira pomwe amasankhidwa pa udindowu akhala akutumikira ku parishi ya Nathenje ngati bambo mfumu ndipo potsatira kusankhidwa kwao, ayamba kutumikira ku bungweli pa 8 mwezi watha.