Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Apolisi M’boma la Mangochi Akusaka Zigawenga Zisanu

$
0
0

Apolisi m’boma la Mangochi ati akufunafuna anthu ena asanu omwe sakudziwika omwe anapita kukaba ndi zikwanje kwa mzika ina ya mdziko la India.

Wachiwiri kwa ofalitsa nkhani za apolisi m’bomali Sergent Amina Daudi watsimikiza za nkhaniyi ndipo wati mzikayi a Imran Yusuf a zaka 35 omwe akukhalira mmudzi mwa Kalonga kwa mfumu yaikulu Mponda m’boma lomweli la Mangochi amachita bizinesi.

Sergent Daudi ati lachinayi madzulo a Yusuf ataweruka anakhala pakhonde la nyumba yao pomwe amacheza ndi banja lawo, ndipo mwadzidzi kunatulukira anthu asanu atanyamula zikwanje ndi nkhwangwa omwe anawuza a Yusuf kuti alowe mnyumba ndipo anakwanitsa kuwalanda ndalama zokwana 2 miliyoni 5 hundred sauzande, makina a computer a laptop komanso foni ya mmanja.

Iwo ati apolisi atadziwitsidwa, apolisi anakawona kunyumbako ndipo padakali pano kafukufuku ali mkati woyang’ana anthuwa.

Anthuwa akapezeka ati akuyembekezeka kukayankha mlandu wakuba mowopseza zomwe ndi zotsutsana ndi gawo 301 la m’buku la malamulo oweruzira milandu.

Apolisi m’bomali achenjeza anthu kuti asamasunge ndalama zochuluka mnyumba pofuna kupewa kuberedwa.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875