Mabungwe osiyanasiyana mu mpingo wakatolika awayamikira kaamba ka ntchito yotamandika yomwe agwira mu mchaka cha 2016.
Wapampando wa mabungwe a utumiki a apapa mdziko muno la Pontifical Missinaries Society (PMS) bambo VincentMwakhwawa ndi omwe anena izi lero ku Lilongwe.
Bambo mwakhwawa ati zomwe achita mabungwewa mchaka chomwe chikupita kumapeto cha 2016 zikugwirizana kwatunthu ndi zimene mtsogoleri wa mpingo wa katolika pa dziko lonse papa Fransisco wakhala akulimbikitsa kuti zizichitika.
Iwo ati mwa zina ma bungwewa akwaniritsa kuchita ntchito za chifundo, kuyanjanitsa anthu amitundu yosiyanasiyana komanso kukwaniritsa kupereka ma lipoti ammene ma parish ngakhalenso ma dayosizi awo agwilira ntchito mchakachi mu nthawi yake.
Pamenepa bambo mwakhwawa alimbikitsa mabungwewa kuti apitirize kuchita ntchito zachifundo komanso ntchito zina zotukula mpingo komanso dziko mu chaka cha 2017.