Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Maepiskopi a Mdziko la America Sakugwirizana ndi Maganizo a Trump

$
0

Bungwe la maepiskopi a mpingo wakatolika mdziko la America la United States Conference of Catholic Bishops latsutsa maganizo a Pulezident wa dzikolo a Donald Trump ofuna kumanga mpanda pa malo omwe panachita malire a dzikolo ndi dziko la Mexico ati pofuna chiwerengero cha anthu ambiri okhala mdzikolo opanda zowayenereza azitha kuwagwira ndi kuwathamangitsa.

Maepiskopiwa apereka uthengawu kudzera mu uthenga omwe atulutsa omwe wasayindidwa ndi wapampando wa bungweli Ambuye Joe Vasquez.

Uthengawu wati mfundoyi ichititsa kuti anthu ambiri omwe anachoka mmaiko awo ndi kukakhala mdziko la America azikhala mwa mantha komanso anthu mmabanja azikhala molekana.

Ambuye Vasquez ati akulemekeza ufulu wa boma, koma sakukhulupilira kuti kumanga mpanda pa malo omwe panachita malire a dzikolo ndi dziko la Mexico ati pofuna chiwerengero cha anthu ambiri okhala mdzikolo opanda zowayenereza azitha kuwagwira ndi kuwathamangitsa, ndi njira imodzi yomanga dziko labwino.

Iwo ati ali ndi mantha kaamba koti ndondomeko ngati zimenezi zichititsa kuti amayi ndi ana azilephera kulandira chitetezo chokwanira.

Pomaliza kalatayi yati ma episkopiwa apitiriza kumanga umodzi ngakhalenso kuthandiza mabanja omwe anachoka mmaiko ena ndi kukakhala mdzikolo.

<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>