Dziko la Columbia lalengeza za mapulani ofuna kuthetsa kulima mbewu ya Coca yomwe amapangira mankhwala ozunguza bongo a Cocaine.
Malipoti a wailesi ya BBC ati alimi amene achotse mbewu zawo okha m’munda mwawo azipatsidwa malipiro mwezi uliwonse komanso azipatsidwa ngongole ndi kuwathandiza maganizo pa mbewu zina zoti ayambe kubzala.
Malipoti ati boma la dzikolo layika padera ndalama zokwana 340 million za America (dollars) zomwe zipindulire mabanja oposa 50 thousand ndipo banja lililonse lizizandira 350 dollars pa mwezi.
Boma la dzikolo ati likufuna kuwononga ma ekala 100 thousand a mbewuyi chaka chino ndi kupeza mbewu zina zoti anthu azilima ndi cholinga chochepetsa kupezeka kwa mbewuyi mdzikomo.