Boma lati ntchito yolumikiza magetsi m’madera akumidzi ikuyembekezeka kudya ndalama zokwana 8 Billion kwacha.
Nduna yoona za chilengedwe komanso mphamvu za magetsi a Bright Nsaka ati gawoli ndi la nambala 8 ndipo unduna wawo uyesetsa kuti anthu mdziko muno maka m’madera akumidzi akhale ndi mwayi okhala ndi magetsi.
Iwo amalankhula izi lolemba lapitali mu mzinda wa Blantyre pomwe amalandira katundu wina othandizira pa ntchitoyi kuchokera ku Cullin Africa.
Ntchitoyi ikuyembekezeka kufikiranso zipatala zina potsatira zomwe phungu wa kunyumba ya malamulo wadera la kumvuma kwa boma la Dedza adapempha posachedwapa m’nyumba ya Malamulo.