Mamuna wina m’boma la Ntchisi ati wafa atamira mu mtsinje wa Bua komwe anapita kukawedza nsomba.
Wofalitsa nkhani za apolisi mbomali Sergent Gladson M’bumpha watsimikiza za nkhaniyi.
Sergent M’bumpha wati mamunayu Samson Yola wa zaka 31 zakubadwa yemwe amadwala matenda a khunyu anapita kokawedzaku ndi mng’ono wake Gaison Yola yemwe anasiya malemuyu ndi kubwelera kunyumba.
Malipoti ati malemuyu sanabwelere kunyumba usiku onse zomwe zinachititsa kuti tsiku lotsatira bambo ake ndi anthu ena ayambe kumuyang’ana pomwe anakamupeza ku mtsinjeki atamira.
Sergent M’bumpha ati akuganizira kuti malemuyu anagwidwa ndi matendawa pa nthawi yomwe amawedza zomwe zinachititsa kuti agwere mu mtsinjemo.
Malipoti a ku chipatala chaching’ono cha Malomo m’bomalo asonyeza kuti malemuyu wafa kamba koti amalephera kupuma.
Malemuyi ankachokera mmudzi mwa Khasu kwa mfumu yaikulu Chilooko m’boma lomwelo la Ntchisi.