Mtsogoleri wa mpingo wa Katolika pa dziko lonse Papa Francisko wati popanda amayi dziko silingasangalatse konse.
Iye amalankhula izi ku mwambo wa nsembe ya Misa ku Santa Marta mu mzinda wa Vatican.
Papa Francisko amanena izi pomwe amalalikira nkhani yokhudza Adam ndi Hava.
Malinga ndi Papa Francisko, ntchito ya amayi sikumangosamala pakhomo ngati m’mene ena amaganizira koma kubweretsa chisangalalo pa dziko.
Iye wati amayi ndi mphatso yapadera ndipo amakometsa dziko mu njira zosiyanasiyana.