Bungwe lomenyela ufulu wa amayi ndi ana amasiye mdziko muno la Foundation for Widows and Orphans (FAWO) lati nthawi yakwana yoti amayi amasiye akhale odziyimira pawokha pa nkhani za chuma.
Polankhula ndi Radio Maria Malawi mu mzinda wa Blantyre, pokonzekera mwambo wa tsiku loganizira ufulu wa amai amasiye pa dziko lonse lapansi, omwe udzachitike pa 28 June mu mzinda wa Blantyre, mkulu wa bungweli a Kenneth Chipeta wati ngati amayiwa akhale odziyimilira pawokha pa chuma atha kukhala ndi kuthekera kothandiza ana omwe asiyilidwa.
“Ana ndi amayi ambiri amadalira bambo amene amakhala akuchita business kapena kugwira ntchito. Ndiye nthawi zambiri bambo akamwalira umakhala ngati mzati wagwa chifukwa ndi amene amakhala akuthandiza banja lake. Udindo wonse tsopano umakhala m’manja mwa mayi wotsala uja monga kulipira sukulu, zovala, chakudya ndi zina zambiri. Ndiye amayi chifukwa amakhala alibe chochita amavutika kwambiri,” anatero a Chipeta.
A Chipeta ati zikhalidwe za dziko lino monga kulowa kufa zikuyika miyoyo ya amaiwa pachiswe. Iwo apempha kuti anthu asamawagwiritse ntchito amayi amasiyewa chifukwa ndi ovutika.
Iwo ayamikira boma ponena kuti likuwonetsa chidwi pa mwambo womwe bungweli likhale nawo posachedwapa komanso makamaka kuti likufuna litagwira ntchito limodzi ndi bungweli pofuna kuthetsa mavuto amene amayi amasiye amakumana nawo.