Amayi ena awiri akuyembekezeka kukawonekera ku bwalo la milandu mawa ndi kukayankha mlandu wokhudzana ndi kuphedwa kwa mchimwene wake wa mtsogoleri wa dziko la North Korea,Kim Jong-Nam.
Malipoti a wailesi ya BBC ati amayiwa Doan Thi Huong wa zaka 28 zakubadwa wa mdziko la Indonesia komanso Siti Aisyah wa zaka 25 wa mdziko la Vietnam ndi ena mwa anthu khumi omwe akuganiziridwa kuti anachita chiwembuchi.
Mkulu woona za malamulo mdzikolo wati amayiwa akapezeka olakwa pa mlanduwu atha kulamulidwa kuti aphedwe.
Amayiwa akuwaganizira kuti ndi amene anapaka mankhwala owopsa kunkhope kwa Kim Jong-Nam pa bwalo la ndege la Kuala Lumpur mdziko la Malaysia, ku mayambiliro a mwezi uno.