Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Papa Wapempha Ansembe Akhale a Chiyembekezo, Chikhulupiliro

$
0
0

Mtsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Francisco wati ansembe akuyenera kukhala a chiyembekezo chabwino mmoyo wao pokumbukira zimene Mulungu anawalonjeza komanso pokhala a chikhulupiliro.

Papa amalankhula izi kwa ansembe omwe anasonkhana nawo ku tchalitchili lalikulu la mu dayosizi ya Rome.

Iye wati chikumbutso cha zimene Mulungu amalonjeza chimatsamira pa zimene mpingo umayembekeza komanso mu chikhulupiliro chimene akhristu eni ake amakhala nacho.

Mwa zina pa mkumanowu ansembewa analandira sacrament la kulapa kudzera mwa mtsogoleri wa mpingo wakatolikayu.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>