BungweMalawi Bureau of Standards (MBS) layamba latseka nyumba zogona alendo za Golden Peacock komanso Pacificmu mzinda wa Lilongwe kaamba koti zikusowa zinthu zina zolimbikitsira ntchito za ukhondo.
Bungweli latseka nyumbazi litamaliza kugwira ntchito zake zoyendera ma hotela omwe akupezeka mu mzinda wa Lilongwe.
Mkulu wa bungweli a Darwin Chokazinga watsimikizira atolankhani a Malawi News Agency(MANA) za nkhaniyi ndipo wati kuyambira pano nyumbazi sizikuyenera kuti anthu aziloledwa kugonamonso pokhapokha eni malowa atazikonza polimbikitsa ntchito za ukhondo.
Iwo ati bungweli lidzapelekanso chilolezo choti nyumba-zi ziyambenso kugwira ntchito pokhapokha zitasonyeza kuti kuti zili ndi ukhondo wokwanira.
Malingana ndi atolankhani a MANA mkulu wa hotela ya Pacific,watsutsa malipoti oti Hotela yawo yatsekekedwa, pomwe eni malo a Hotela ya Golden Peacock anakana kuthililapo ndemanga pa nkhani-yi.