Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Asisteri Anayi Afa pa Ngozi mdziko la Ethiopia

$
0
0

Asisiteli anayi afa ndipo ena atatu avulala modetsa nkhawa pa ngozi ya galimoto mdziko la Ethiopia.

Malingana ndi malipoti a Catholic News Agency (CNA), a sisiteliwa omwe ndi achipani cha Daughters of St Anne amapita ku maliro mu mzinda wa Hawassa a m’bale wake wa mmodzi mwa asisiteliwa.

Asisiteliwa akhala akugwira ntchito zosiyanasiyana monga kuyang’anira sukulu, zipatala, sukulu yophunzitsirako zolukaluka, malo osungilako ana amasiye, komanso kuyang’anira sukulu ina yomwe anthu osaona ndi ina yophunzitsilako ntchito za manja.

Chipani cha Daughters of St Anne chinayamba kugwira ntchito mdziko la Ethiopia kuyambira mchaka cha 1968.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875