Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Dziko la Guatemala Litaya Atsikana Makumi Awiri pa Ngozi ya Moto

$
0
0

Dziko la Guatemala lakhazikitsa masiku atatu okhudza maliro a atsikana makumi awiri omwe amwalira kaamba ka moto omwe unabuka pa malo ena osungirapo ana mdzikolo.

Malipoti ati atsikana omwe amwalirawa ndi a zaka za pakati pa 14 ndi 17 ndipo ambiri mwa iwo afa ati kaamba koti anapsa kwambiri. 

Malinga ndi malipoti motowu unabuka kaamba ka mattress omwe anayatsidwa ku malo omwe atsikanawa amagona.

Mmodzi mwa anthu omwe amagwira ntchito pa malowa a Angel Cardenas ngozi ya mtunduwu si yachilendo kaamba koti malowa amasungira ana ochuluka kuposera chiwerengero choyenera.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>